Vote For This Song

Lyrics

Intro Haaaa!!! Yah know its ah Warrant Officer Class 1 General Lic, (Classic) Ondilangiza analipo aaaah/ Sinnamvele malangizowa/ Ndinakomedwa nawo abambowa/ Osadziwa angondi user nkundipotokola/ Chorus Ondilangiza analipo koma kusamvaaa/ Banja ili n'lazigawenga ndipo n'lambavaaa/ Ndilopanda chisoni anthu ake ndi ankhanzaaa/ Chifukwa chakusamva andisiya mmasanzaaa/ Verse 1 Ankaonetsa umuthu pofuna kundikwatira/ Kulikonse uko ndingapite iye ankandisatira/ Akazi ena omufuna simomwe ankawasasila/ Osadziwa ufumu wakwathu ndiomwe ankausatira/ Chongonditenga ufumu napasidwa/ Chikondi chinachepa chomwe ndinkapatsidwa/ Anayambika mavuto nyumbamo/ Kuiwala Mgwilizano kudana nchilungamo Anayamba kundisakaa (eheee)/ Zimilandu kundipakaa(oohoo)/ Kukhala chete ndinasakhaa/ Nditangodziwa nduyendedwa ngati (ma card)mpaka/ BTC Verse 2 Zinayambika ngat macheza/ Kenako kuyamba kutukwanika ndi ana owapeza/ Akakhala ntimagulu basi kuma opsyezaa/ Apa mpomwe bondo ndinanong'oneza/ Anayamba kundipangila ma upo/ Zimilandu mpaka pa bwalo pa amfumupo/ Ndinalira misozi ndikukhetsa/ Amuna anga achakhuli kwa ana anu mundiphetsa/ Ndawalira a x anga a petulo/ Kuyambana ankasiyabe ndalama ya ndiwo pa tebulo/ Ndinkafuna kuwala pano nduchita kusowa ya kendulo/ Katatu sitingadye mulibe ufa okwana mudengulo/ Nnakomedwa ndipakamwa podya za nchele/ Ndinkati uyu ngwa banja osadziwa angofuna andibele/ Nkulingadi utayenda naye kuti udziwe alidele/ Komabe family flag yakwathu ndiyo ndidzafele/ (BTC) (Bridge) Anayamba kundisakaa (eheee)/ Zimilandu kundipakaa(oohoo)/ Kukhala chete ndinasakhaa/ Nditangodziwa nduyendedwa ngati (ma card)mpaka/ BTC ×2

Sharing is cool

You may also like...



Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Comments
Hits 1836 Plays. | 984 Downloads.

Follow Malawi Music on Instagram