Vote For This Song

Lyrics

Chorus x2
Yakwana nthawi ya bwana (Wa ku State House)//
Ifeyo tadikilia kokwana (Wa ku State House)//
Tinatopa ife ndi za chibwana (Wa ku State House)//
Yakwana nthawi ya bwana (Wa ku State House)//

Verse 1
Tiubwerapo anuwake a DPP
Munali ongobwerekela inu a PP
Timapikisina ife ndi MCP
Amai simunalinso pafupi
Tbwera ife anuwake boma
Ife zimatisowa ife ndalama
Amai munachulutsa za drama
Ineyo pan mwina ndiyenela beemer!

Chorus x2

Verse 2
Yakwana nthawi ya Mutharika
Amai kodi zikuvutani kutsazika?
Kapena tizakuthandizeni kusamuka?
Mapeto ake amai mungoyaluka
Azibusa kapitilizeni kulalika
Ngati za ndale ziku kanika
Anthu anu nde aku tayika
mudzalamulia nthawi yanu ikadzafika

Chorus x2

Verse 3
inasokonekera atamwalira a Bingu
Dziko analitenga ndi anthu osenza ma dengu
Ine kunyumba ndimangogonela mawungu
Ndikadya za nkhiwru ndinkadya mphalabungu
Mwina ikonzedwenso miseu
Amai mumangochulutsa mihawu
Makani ngati ndinu munthu wa Nyau
Amai inuyo mulibenso mawu

Songwriters

Gibo Lantosi, Wanangwa "Warge" Phiri

Sharing is cool

You may also like...



Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Gibo Lantosi hooks up with the massive Warge Records sound system pon dis State House Riddim.

Comments
Hits 25433 Plays. | 19137 Downloads.
« Sugar Mummy Dolo Wa Mu Hood Songs Ma Units »

Follow Malawi Music on Instagram