Vote For This Song
Lyrics
Ndinaleledwa ndi mphuzitsi Kubadwa kukula mpaka kumaliza sukulu Sitinakhale ndi nthawi zachimwemwe zochuluka Koma Mulungu anali yathu mbali Mayi anga anali mphuzitsi Tsiku ntsiku ankakhala pansi Kulemba ma scheme ndi ma lesson plan Chuma chawo chachikulu chinali njinga Kupalasa mitunda yaitali tsiku ntsiku Ntchito yomwe ngati dziko tinasankha kuyiyang'anira pansi Koma sanaleme mayi Chaka nchaka kutumiza ana ku ma secondary odziwika Akakhale mabwana omwe adzapitilize kunyoza aphunzitsi Kuwatukwana ngati palibe chomwe amadziwa Kuwapondereza kuwatukwana nkuwayankhula zachabe Mayi anga anali mphuzitsi Akawerengera ngongole zawo pena ankalira mayi Ana asanu ndi mmodzi adyanji malipiro osakwanira Ntchito yopanda ma workshop zaka mpaka makumi awiri osakwezedwa olo Yehova nde m'busa wathu sitizasowa ndiye inali yathu nyimbo tsiku ntsiku Lero tadya mawa nlachauta ndiye unali moyo wathu Mayi anga anali mphuzitsi Nyumba zathu zambiri zinkakhala za pa sukulu zomwe ankaphunzitsapo mayi Nyumba zodontha, zitseko zosakiyika zosamilitsira mipando mayi Mipandoyo kukhala nayo ankakhala katapila mayi Koma tsiku ntsiku tinkawaona ndi zochonga zambiri akuchonga mayi Ndithu pokonza tsogolo la chigulu sankanyinyirika mayi Chikakhale mmaofesi aulemelero chigulu Kuti mapeto ake chidzawatukwane bwino mayi Kuvala zovala zanyuwani ngati ana amphuzitsi pankakhala pa khirisimasi basi Nsapato za pulasitiki pena makabudula ong'ambika Chanzeru ku secondary popita tinkatenga chili chokazinga chimanga Pena musakazinge chambiritu baba tingalowe munjala akuchondelera mayi Koma chaka nchaka akusema tsogolo la aanthu amene adzakhale mabwana nadzakhale opanda nawo ntchito aphunzitsi mayi Mayi anga anali mphuzitsi Nde mayi ndi malipiro awo ochepa ankakwanitsa kutigoneka pa nkeka basi Blangete loperepeseka kumafunda ana awiri awiri Olo ndalama ya pillow sankakwanitsa Mbale za pulasitiki zina zowotchedwa ndi moto wankhuni Madzi kotunga kunkangokhala ku mjigo, Magetsi sitinawadziwe Palibe chuma ndingazakusiyireni ankatiyankhula misonzi ili mmaso Chuma ndingakupatseni ndi maphunziro omwewa Pamene nduphunzitsa ena nanu phunzirani Mudzakhale pabwino nimuzadyelere Kwa ine kwatha ngati mphuzitsi Nzakondwera ti makatapira ndutengati titakupindulirani Njinga yakapalasa ndimapalasa itakubalirani magalimoto Koma kuti moyo wathu aphunzitsi nkuzasintha nzokaikitsa Mphatso yanga ana anga ndi maphunzirowa Ndi kusaiwala Mulungu ndinso Kudzichepetsa Lero mayi anapuma Mphavu zinapita njinga sangapalase Pension yawo kuyiona mutha kulira Moyo wa iwo ndaphunzitsi anzawo omvetsa chisoni Mu ukalamba wawo alibe medical scheme Zinthu zinadhula pension sikwana Nthaka inaguga koma feteleza pawokha sangakwanitse Chipumileni mayi zambiri zasintha Maboma abwera nkupita Koma mnyozo kwa aphunzitsi sunathe Ulemu kwa maphunziro sitinayambebe kupereka Otonzedwa, otukwanidwa, oyang'aniridwa pansi ndi mphuzitsi Zamisonzi yawo sizimveka Mapempho awo ndi phwete kwa odzitcha okha ozindikira Kudeleredwa ndi ana ndi asukulu komiti kosayamba Salary, pension zachisoni Ntchito zopanda allowance Nkamaona izi misonzi imatsika Chifukwa nzomwe ndakula nazo Ndipo simungandinamize kalikonse ka mphuzitsi anta Nkofunika tikanasintha Kupereka ulemu kwa onga anga mayi aphunzitsi Kutenga maphunziro ngati chofunika kuposa zonse Bajeti maphunziro kumalandira kuposera kalikonse Osayiwala palibe zaumoyo, zaulimi, zachilichonse zopambana opanda maphunziro Koma mwina mwa nthawi zonse ndakatuloyinso simukhala nayo attend Poti ikukamba za ulemu kwa mphuzitsi Koma kwa tonse amene takulira mnyumba mwa mphuzitsi Sitingayankhule mtudzu olo pang'ono Ma Pempho awo olo atakhala osatheka mu nthawiyo Sitingawayankhule mobwafula Anthuwa akumana nazo ndipo amakumana nazo zokhoma Osaiwala sindikungoyankhula Mayi anga anali mphuzitsi |
Sharing is cool
You may also like...
Mobile Site
Review
Comments
