Vote For This Song
Lyrics
Chorus Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tisauke Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tivutike Verse 1 Malawi dziko langa lokondeka ah Lomwe ndinalikonda ndili mwana ah Koma zambiri zapotoka Zaloza kuzende Chonde mbuye, unikilaaanipo Chuma chathu ngati dziko mchofooka Anthu ambiri dziko langa ngaumphawi Mene muchilitsa China Mudalitsa America Naye Malawi mumkumbukireee Chorus Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tisauke Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tivutike Verse 2 Zotupa zamubongo komaso m`mimba ah Bp cancer komaso sugar ah Imfa za amayi apakati Ana ogwiliridwa, odwala edzi muakhudze ndinuuuu mbuye Sambitsani misewu yathu ndi mwazi wanu mbuye Ngati tachoka amoyo tikafike Dalitsani atsogoleri, amipingo azipani atilamulire Umo mufunila halleluyah Ndikamaliza ntchito yanga, yoimbayi Ndizatseka maso, ambuye adzandiitana Ndiye otsalanu, musazatope, kumpemphelera Malawiii Chorus Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tisauke Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tiyaluke Bridge Mbuye malaawii Dziko langa, dziko langa Dalitsani Malaawii Dziko langa, dziko langa Chorus Ndife ana anu Ndife ana anu Msatilore tisauke Ndife ana anu Ndife ana anu Msatiloere tivutike |
Sharing is cool
You may also like...
Mobile Site
Review
Comments
