Vote For This Song
Lyrics
Chorus Akhristu ambiri lero amapembedza Selofoni Akhristu ambiri, Mulungu wao ndi Selofoni VERSE 1 Akakhala pa nyumba, amakhalira pa selofoni Samacheza ndi ana, tsiku Lonse pa selofoni Akakumana ndi vuto,mmalo moti apemphere, Amakalemba pa fesibuku, Mulungu wao ndi Selofoni Kaya akupalasa njinga, nkono wina pa Selofoni Akafika ku ntchito, amatenga Selofoni Ayambe kumvera nyimbo, nyimbo zosalongosoka Ndekuti tsiku lonse woye woye woye woye kuba nthawi ya ofesi ambuye Chorus Akhristu ambiri lero amapembedza Selofoni Akhristu ambiri, Mulungu wao ndi Selofoni VERSE 2 Popita ku chalichi, samaiwala Selofoni Amalisiya Baibulo, koma osati Selofoni Abusa akulalikira, iwo ali pa fesibuku Uku akugwedeza mutu, koma sitili limodzi (Selula foni) Leo machalichi akudzadza, koma omvetsera ndi ochepa Anthu ambiri maganizo ali kutaaaaaaaaali bridge Zalowa chibwana, chibwana cha mchombo lende Zalowa chibwana, Ngati inakufera pa mtanda Zalowa chibwana, Pa mtanda Selofoni Zalowa chibwana, VERSE 3 Kachinthu kofunikira, ukakagwiritsa ntchito bwino Anthu akupeza mabanja, mbalume pa selofoni Mabanja ena kutha kumene, nkhani yake ya Selofoni Mautumiki akutha kubadwa, kutumikira pa selofoni Isatidyere nthawi ya pemphero, isalande malo a Yehova Tachezaniko ndi akazi wanu, lero lokha foni ipume Isatidyere nthawi ya pemphero, isalande malo a Yehova Inu tachezaniko ndi amuna anu, lero lokha foni ipume OUTRO Akhristu ambiri lero amapembedza Selofoni Zalowa chibwana Akhristu ambiri, Mulungu wao ndi Selofoni Zalowa chibwana FONI SELULA FONI!!! |
Songwriters
Faith Mussa, Don FoxxySharing is cool
You may also like...
Mobile Site
Review
SELOFONI – WRITTEN BY FAITH MUSSA. Produced at Step Up Records by Faith Mussa and Don FoxxyComments
28921 Plays. | 43647 Downloads.